
Pomwe aMalawi ambiri akudandaula ndi kukwera kwa katundu osayinasiyana m’dziko muno, kampani ya Illovo Sugar yakwezanso mtengo wa sugar.
Malinga ndi kampaniyi paketi ya sugar ya 1kg tsopano izigulitsidwa pa mtengo wa K3000.
Kampaniyi yati kukwezaku kwadza chifukwa cha kukwera kwa mitengo ya zipangizo zopangira sugar ndi zina.
Ngakhale kampaniyi yakweza sugar pa mtengo wa K3000, mu ma shop ena sugar akugulitsidwa k4000, ndipo ma shop enanso sugar sakupezeka.
Pamene zinthu zikupitilira kukwera m’dziko muno, Boma la Chakwera silikuwonetsa chidwi chothana ndi vutoli, ndipo chodabwitsa ndi chakuti akuluakulu ena a chipani cholamula cha Malawi Congress monga a Jessie Kabwira akumati zinthu m’dziko muno zikukwera mtengo chifukwa cha chipani chotsutsa cha DPP.