Akakhala ku ndende zaka zitatu kamba kovulaza ng’ombe za eni

Advertisement
Court

Oweruza milandu, First grade Magistrate Court m’boma la Karonga wagamula bambo Tey Mwanguku a zaka 40 kukakhala ku ndende zaka zitatu akugwira ntchito ya kalavula gaga kamba kopezeka olakwa pa mlandu ovulaza ng’ombe ziwiri zimene zinaononga munda wawo wa mpunga.

Mboni ya boma pa mlanduwu, Inspector Jennifer Chawinga wati pa 3 March, 2025, ana a gogo yemwe ndi mwini ng’ombezo anawaona bambo Mwanguku ali ndi mpeni wamagazi akuchokera ku khola la ziwetozo.

“Ana atafika ku kholako anapeza ng’ombe zo zikutuluka magazi miyendo yake ndipo zimalephera kuyenda.

Anawa anaitana gogo wawoyo yemwe anaitengera nkhaniyi ku polisi ya Songwe ndipo apolisi atafika pamalopa limodzi ndi alangizi aziweto, anapeza kuti ng’ombezi zinavulazidwa kwambiri kotelo sizingakhaleso moyo,” anatero a Chawinga.

Ataonekera ku bwalo la milandu pa 10 March 2025 , Mwanguku anavomera mulanduwu ndipo anapempha bwaloli kuti lichepetse chigamulo kamba koti ng’ombezi zinaononga munda wake wa mpunga.

Koma oweruza milandu wagamula bamboyu kukakhala ku ndende zaka zitatu kamba kovulaza ziweto zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 343 ndime yachiwiri ya Malamulo a dziko lino.

Mwanguku ndi ochokera m’mudzi wa Mwandenga mfumu yaikulu Mwakaboko m’boma la Karonga.