AMalawi mukuwamana Vitamin A – Namiwa


Namiwa

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu anthu mdziko muno la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), Sylvester Namiwa wati aMalawi akumanidwa Vitamin A ndi michere ina yomwe imapezeka mu Suga ndipo ndi yofunika kwambiri chifukwa cha ukambelembele omwe wazungulira malonda a Suga mdziko muno.

A Namiwa awuza nduna yowona za malonda a Vitumbiko Mumba kuti ichitepo kanthu ponena kuti mdziko muno mavuto a kusowa kwa Suga amachitika chaka ndi chaka maka kuyambira January kufika June ngakhale kampani yopanga Suga ya Illovo imalengeza phindu lochuluka zomwe zutanthauza kuti imapanga Suga okwanira.

Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani mu nzinda wa Lilongwe lero, a Namiwa ati Suga ndi chinthu chofunika kwa munthu chifukwa mumakhalanso Vitamin A yemwe ndi ofunika kwambiri mthupi la munthu ndipo kukwera kwa mitengo ndi nkhawa pa aMalawi chifukwa kutero ndi kuwamana aMalawi Vitamin A.

Mkulu wa bungweyu watinso nzomvetsa chisoni kuti ku mayiko a kunja Sugayu amapita pa mitengo yabwino kulekana ndi kuno kumudzi komwe Sugayu akupangidwa ndipo ati ma umboni alipo pomwe ati nthawi yakwana tsopano kuti Illovo idzifotokozera momveka bwino pa m’mene imabwelera ndi mtengo odula pa Suga wa kuno .

A Namiwa atinso yemwe ali nduna ya maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda akukhalira zotsatira za kafukufuku okhudza kusowa kwa Suga yemwe anachitika mu July 2023 ndipo ati a Vitumbiko Mumba achitepo kanthu.

Iwo atinso nduna Vitumbiko Mumba ikumbukire kuti nkhani yothana ndi kusowa kwa Suga imakhudza ‘Cartel’ (chi mlambala/gulu la anthu amene akupanga zinthu limodzi)

Posachedwapa nduna Mumba inatsogolera limodzi ndi mabungwe ena kupita ku Sitolo ya Chipiku komwe anakapeza akulu akulu atabisa Suga koma amauza athu kuti Suga watha mu sitoloyi ndipo pa alumale padalibenso

Pambali pa Vitamin A, mu Suga mumapezekanso vitamin C, B1 mpaka B6, Calcium, Magnesium, Potassium, Iron, ndipo zimathandiza kwambiri kuti munthu adziwona bwino, kupereka mphamvu, kuchiza mabala mosavuta, komanso umoyo wa mwana yemwe sanabadwe mwa zina.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading