Kalisto Pasuwa wayamba kutumikira zofuna aMalawi

Advertisement
Flames

Mphunzitsi wa Flames yemwe wangolembedwa kumene Kalisto Pasuwa wayamba ntchito yake ndi chipambano pomwe wawaula Comoros 0-2 mu mpikisano wa African Nation Championship Qualifiers pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.

Zigoli za Binwell Katinji ndi Zebron Kalima mzigawo zonse ziwiri ndi zomwe zapatitsa ma points onse timu ya Malawi the flames kuti ipite moyenda ndi mdidi.

Masewelo a lero Flames inali koyenda ngakhale imasewela mdziko lake lomwe kutsatira chisankho chomwe Comoros inachita kuti asewelera masewelo ake kuno ku Malawi.

Flames isewera masewelo ake a chibweleza loweluka pa bwalo lomweli la Bingu ndipo ngati ingapambane idzakumana ndi ma timu a pakati pa South Africa ndi Egypt mu ndime ina.

Kalisto Pasuwa anayambitsa George Chikooka pagolo, MacDonald Lameck, Maxwell Paipi, Lloyd Aaron, Nickson Mwase, Yankho Singo, Gaddie Chirwa, Binwell Katinji, Alick Lungu, Ephraim Kondowe ndi Wisdom Mpinganjira.

Bungwe la Football Association of Malawi (FAM) lidalemba mphunzitsi wakale wa FCB Nyasa Big Bullets- yu pa kontalakiti ya zaka ziwiri ndipo aMalawi ambiri ayamikira ntchito za Pasuwa.