Zathera panjira: Zelenskyy wachoka pa mkumano ndi Trump atasemphana chizungu

Advertisement
Donald Trump - Volodymyr Zelenskyy

Mkumano wa mtsogoleri wa dziko la America a Donald Trump ndi mtsogoleri wa dziko la Ukraine a Volodymyr Zelenskyy wathera panjira pomwe akulu akulu awiriwa athilana mawu.

Mkumanowu unakonzedwa ndi cholinga choti mayiko awiriwa akakambilane za momwe angaimitsire mtsogoleri wa dziko la Russia a Vladimir Putin kuthira nkhondo dziko la Ukraine.

Ngati mbali imodzi yoti dziko la America ithandizire izi kuchitika, dziko la Ukraine limayeneranso kusaina mgwirizano ndi a Trump opereka ma minerals ake ku dziko la America.

Koma m’malo mwake, izi sizinatheke kamba kakuti Trump, komanso wachiwiri wake JD Vance, anapitiliza kukalipira a Zelenskyy powauza kuti alibe ulemu komanso sanathokozepo angakhale kuti dziko la America lakhala likupereka ndalama zankhaninkhani kudzera mu utsogolore wa a Joe Biden pothandizira nkhondo yapakati pa Ukraine ndi Russia.

A Trump anawuza Zelenskyy kuti alibe mphamvu yolamura zomwe akufuna kamba kakuti nkhondo yomwe a Putin akuthira dziko lake yafika poyipa ndipo palibe tsogolo loti atha kupambana nkhondoyo popanda thandizo la America.

A Trump anapitiliza kuopseza a Zelenskyy kuti makani akupangawo, sawapindulira chifukwa zomwe akuchitazo nkushosha nkhondo yachitatu ya dziko lonse.

A Trump anauza a Zelenskyy kuti zikuonetseratu kuti iwowo sanakonzeke kuti maiko a Russia ndi Ukraine akhale pa mtendere ndipo ngati akufuna kutero, adabwerenso ku America akadzakonzeka kuti maiko awiriwa akambilane ncholinga choti nkhondo ithe.

Monga momwe zimakhalira mwa nthawi zonse a Trump akaitana atsogoleri a maiko ena kuzokambilana pomwe amayankhura osayankhidwa, izi sizinali chomwechi kamba kakuti a Zelenskyy amayankha ndipo anamuwuza Vance kuti “kodi ndi ulemu wanji omwe inu mukufuna kuti tipereke ku dziko lanu? Chiyambileni nkhondoyi, takhala tili tokha, nde inu mukutinji? Ulemu wake wa mtundu wanji?

Izi zinakwiyitsa a Trump ndi achiwiri awo omwe anauza a Zelenskyy kuti “inu ndi mtsogoleri wa nkhanza ndipo mukuyenera kuzengedwa milandu ya nkhaza kwa anthu anu. Ndinunso opanda ulemu maka maka kwa ife a dziko la America ndipo dzipitani, mukadzakonzeka, mudzabwera, musatitayitse nthawi”.

A Trump anapitiliza kuwuza Zelenskyy kuti “sainani apo bii, sitikuthandizaninso”

Apa a Zelenskyy anakanilatu kusaina mgwirizano ndi America ofuna ma minerals awo ponena kuti zinali zopanda nzeru kulowa mu mgwirizano omwe sukupereka masomphenya owonetsa kuti dziko la Russia silidzayambanso nkhondo ndi dziko la Ukraine.

Msonkhano wa atolankhani omwe dziko la America linakonza kuti anthu achitire umboni osaina mgwirizanowo, awulepheretsa kamba kakuti mkumanowo, sunathe bwino.