
Nzika za mudzi wa Ng’onga, dera la mfumu yaikulu Nsamala ku Balaka zomwe zikukhudzidwa ndikugulidwa kwa malo ndi kampani ya Portland Cement Limited, ati Lachinayi lino ayamba m’bindikilo ku khonsolo za bomali.
Izi ndi malingana ndi kalata yomwe nzikazi zalembera mlembi wa unduna wa maboma ang’ono, ofesi ya bwanamkubwa komanso mkulu wa a polisi m’bomali kuwadziwitsa za m’bindikilowu.
“Monga mukukumbukira pa 13 February, 2025 tidapanga zionetsero za bata ndi mtendere zomwe cholinga chake chinali kukakamiza ofesi ya mlembi wa unduna wa maboma ang’ono kuti usamuse a DC aku Balaka, bwana Tamanya Harawa. Ndiye popeza mwanyozera, ife ngati nzika zokhuzidwa ndikutengedwa kwa malo a m’mudzi wa Ng’onga, T/A Nsamala, Balaka; Tibwera ku ofesi ya a DC ndipo tiyamba kuchita m’bindikiro kufikira mutagonjera zofuna zathu kuti muwasamuse a DC apanowa,” yatelo mbali ina ya kalatayi.
Anthuwa omwe akuloza chala Harawa kuti akupondereza chilungamo pa nkhani yawoyi, atinso pa nthawiyi atseka misewu yonse yopita kumalo komwe anasamutsidwa komwe kampani ya Portland Cement ikumanga fakitale. “A Portland Cement samayenereka kugwira ntchito kumene kuja pokhapokha titamvana ndipo titalandira chipukuta misozi choyenera.”
Iwo ati apanga izo ndicholinga chofuna kuti kupite anthu ena oima pawokha kuti akawunikirenso za ndalama zimene iwo ayenera kulandira, ndipo ati adzachoka ku maofesi akhonsoloyi pokhapokha mavuto awo onse atakonzedwa kuphatikizapo kupatsidwa ndalama zawo zoyenera.
“Timangofuna kuti tichenjeze kuti zonse tizipanga mwa bata ndi mtendere ndiyeno pasakhale mchitidwe ofuna kuwopsezana kapena kupanga njomba mwanjira ina iliyonse,” zawonjezera nzikazi. “Ife tili ndi chikhulupiliro kuti mukudziwa bwino kuti kalatayi ndichidziwitso osati kuti tikupempha chilolezo.”