
A George Chaponda mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma mnyumba ya malamulo, ati akupepesa onse amene anabwera lachisanu kudzamvera State of the Nation Address (SONA) yomwe a mtsogoleri wa dziko Lazarus Chakwera anapeleka.
A Chaponda ati anthuwo akanatha kutenga nthawi yawo kupanga zinthu zaphindu ku madela awo kuposa kumvera za ndale zomwe a Lazarus Chakwera amanena mnyumba ya malamulo.
A Chaponda afotokoza izi mnyumba ya malamulo lero pomwe aphungu akukumana kuyamba kulankhulapo pa zomwe mtsogoleri wa dziko anafotokoza zam’mene dziko lilili- SONA
A Chaponda ati mtsogoleri wa dziko waphonya mwayi ofotokozera za mavuto amene dziko lino likudutsamo ndipo ati, aMalawi a mchigawo chapakati atafunsidwa kuti moyo ulibwanji, kodi angakhonze kuvomeleza kuti zinthu zili bwino?.
Iwo ati aMalawi ndi omwe angaweluze za komwe dziko likupita.