
Wamkulu wa amayi kuchipani cha DPP, mayi Mary Thom Navicha wati anthu m’dziko muno atopa ndi mavuto omwe boma lilipo panoli lawayika, ndipo ali pa moto chifukwa MCP ikukanika kupeza njira zothetsela mavuto omwe akuta dziko lino.
A Navicha analakhura izi dzulo mu nzinda wa Lilongwe kumwambo omwe azimayi a chipani cha DPP m’chigawo chapakati anakonza.
Polakhura pamwambowu a Navicha anati chiyembekezo cha aMalawi chili mwa Arthur Peter Muntharika, ndipo aMalawi ambiri akuwona kuchedwa kuti pa 16 September pafike achotse boma lolephera la MCP.
“Lero timakumana ndi azimayi a chipani mu chigawo chapakati kuwawuza kuti asataye mtima kusintha kukubwela ndi Arthur Peter Muntharika. Inu a Malawitu akuvutika kwambiri zinthu zikungokwera tsiku ndi tsiku. Mu ulamuliro wa a Muntharika moyo unali bwino ndipo a Malawi amkasangalala komatu sipano zinthu zafika povuta posautsa thumba la chimanga 90,000 kwacha, kodi munthu wakumudzi wosauka angakwanitse kugula thumba la chimanga pa mtengo umenewu?,” anatero a Navicha.
Malingana ndi a Navicha utsogoleri omwe ulipowu wa Kongolesi ukuwoneka kuti sukulabada zoti a Malawi akuvutika, akulira zomwe zili zomvetsa chisoni kwambiri,” anatero a Navicha.