Zamanyazi: Chakwera wanamiza mtundu wa Malawi, ku Phalombe sikunamangidwe nyumba 29 za Polisi

Advertisement
Chakwera

Zadziwika kuti m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera lero wanamiza a Malawi ku nyumba ya malamulo pomwe anati Boma lake la kongelesi lamanga nyumba 29 za a Polisi mu m’boma la Phalombe.

Koma khonsolo ya bomali yakana kwa mtu wagalu kuti zomwe wakamba Chakwera ndi zabodza zedi, chifukwa mu bomalo mulibe ngakhale nyumba imodzi ya a Polisi yomwe boma la Chakwera lamanga.

Malingana ndi mkulu wa bomali a Agason Sompho, khonsoloyi inangowuzidwa kuti boma likufuna kumanga nyumba za a chitetezo, ndipo pakadali pano palibepo ngakhale nyumba imodzi yomwe yamangidwa.

A Vincent Mkamanga a Phalombe Civil Society Organisation, ati anadabwa ndi nkhaniyi chifukwa chomwe akudziwa iwo ndi choti boma la Chakwera lidangolonjeza kuti limanga nyumbazi koma mpaka pano palibe chachitika.

Anthu ambiri akuti zamanyazi m’tsogoleri wa dziko kunama chotere.

A Chakwera lero anagundika kunyumba yamalamulo kufotokoza zitukuko zosiyanasiyana zomwe boma lawo lapanga mu ma Boma a m’dziko muno.