Nane sindikudziwa, ndili ndi mafunso opanda mayankho – watelo Chakwera pa za imfa ya Chilima

Advertisement
Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati nayenso ali ndi mafunso opanda mayankho pa za imfa ya yemwe adali wachiwiri wake a Saulos Chilima pa ngozi ya ndege mu nkhalango ya Chikangawa ngati momwenso Mary, mkazi wa malemuwa, alinso ndi mafunso opanda nawo mayankhowa.

Mu uthenga wake lero pomwe amatsekulira nyumba ya malamulo, Chakwera wati, Chilima adali munthu olikonda dziko lake ndipo imfa yake idamukhudza iye. Apa mtsogoleri wa dziko linoyu wati monga anthu ambiri, naye ali ndi mafuso osowa mayankho.

“Mausiku awiri okha apitawo, tinakumbutsidwa mwamphamvu ndi mayi Mary Chilima mwiniwake za momwe zimawawira kukhala ndi mafunso omwe Atate wathu wakumwamba yekha ali nawo amayankho pa zomwe zinachitika pa ndege ija isadagwe,” watelo Chakwera.

Chakwera wadandaulaso kuti dziko lino likugawanika chifukwa chofuna kulowetsa ndale komaso kulozana zala pa ngoziyi yomwe idachitika pa 10 June, 2024. Iwo ati izi zapangitsa kuwonjezera chisoni pa mabanja 9 omwe adakhudzidwa ndi ngoziyi.  

Lachitatu pomwe amakhazikitsa SKC Foundation, Mary adauza mtundu wa Malawi kuti akadali ndi mafunso ochuluka pa imfa ya a Chilima makamaka mzomwe zinachitika m’mmaola 24 ngoziyi itachitika kumene.