
Mayi Mary Chilima wati adakali ndi mafunso ochuluka pa zomwe zinachitika maola 24 ku Chikangawa komwe wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino a Saulos Klaus Chilima ndi anthu ena 8 anafa pa ngozi ya ndege.
“Ndikadakonda nditadziwa zomwe zinachitika pomwe Saulos ndi anthu ena 8 anafa pa ngozi ya ndege. Kodi ndi chifukwa chani Saulos, munthu wachikondi komanso wokonda mtendere anafa chonchija?,” anatero a Chilima.
Chipani cha UTM chati sichidapite ku mwambowu pa chifukwa choti boma silinawapatse mayankho omveka pa zomwe zinachitika ku Chikangawa pa 10 June, 2024.
Miyezi iwiri yapitayi komiti yomwe adakhazikitsa m’tsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera idatulutsa zotsatira za kafukufuku yemwe adachita pa zomwe zinachitika pa 10 June, 2024.
Mwazina komitiyi idati ngoziyi inachitika chifukwa cha nyengo yomwe sinali bwino patsikuli.