
Anthu ena a midzi ya group village head Kabiyo ku Ulongwe m’boma la Balaka, ati njala yafika posawuzana pomwe ati Chimanga akugula kapu K900 pomwe chigoba K9000.
Malinga ndi ulendo omwe Malawi24 inali nawo Lolemba, kupita mu delari anthu ena ati akumasungunulabe juwisi wa ma pakete kuwiritsa kuti amwe ndi kugona.
Kafukufuku wathu wapezanso kuti anthu ena akuchita ukapsyala pongongozetsa ndalama zokwana K25,000 kwa anthu ovutikawa ndi cholinga choti akakolora Chimanga adzabweze thumba la Chimanga limodzi, ngakhale pakadali pano thumba la Chimanga la 50Kg lafika 90,000 Kwacha.
Malinga ndi a Benjeman a m’mudzi mwa Chiphwafu, ati anthu ena mderali akumakwanitsa kugula Chimanga ma kapu awiri kugayitsa ndi kuphika nsima kamodzi, ndipo ati ndalama ikuvuta kupeza chifukwa ma ganyu akusowa pakadali pano.
A Naphiri a m’mudzi omwewu apempha adindo kuti ngati nkotheka ayendere delari lomwe anthu akuvutika ndi kuwagawirako chimanga kapena ufa kuti moyo ubweleleko pamene akuyembekezera kucha kwa chimanga.
Mfumu Chiphwafu inavomeleza kuti mdera lake anthu akuvutika ndi njala.
Titapita pa msika wa Balaka Turn-off, tinapeza ogulitsa chimanga m’modzi ndipo kapu inali pa mtengo wa 900 Kwacha pomwe chigoba 9000 Kwacha, pa mphindi zonse zomwe Malawi24 inali pa malo ogulitsira chimangachi, ochuluka ndi omwe amayezetsa chimanga mu ma kapu, awiri atatu kapena asanu ndipo m’modzi yekha anagula chigoba.
M’mawu awo omwe amatulutsa tsiku ndi tsiku m’modzi mwa omenyera ufulu mdziko muno a Bon Kalindo, ati nzomvetsa chisoni kuti boma komanso ma bungwe ena omenyera ufulu akungoyang’ana kukwera kwa mitengo ya dzithu kuphatikiza chakudya ndipo ati pakadakhala ndondomeko zapadera zotchingira kukwera kwa mitengo ya zinthu.
Ukafika mwezi wa February anthu amakhala ayamba kudya chimanga chachiwisi kuchokera ku minda ndi kupulumuka ku njala, koma chaka chino izi zikhonza kuchedwerapo chifukwa cha mvula yomwe inagwa mochedwa mu nyengo ya ulimi wa chaka chino.