
M’tsogoleri wotsutsa boma ku Nyumba ya Malamulo George Chaponda, wati bilu yomwe imafuna kupita ku Nyumba ya Malamulo yoletsa munthu yemwe wafika zaka 80 kuyimira pa udindo wa m’tsogoleri wa dziko lino sipitanso ku nyumbaku.
A Chaponda atsimikiza za izi pa tsamba lawo la mchezo atamaliza mkumano wa business committee omwe umachitikira ku nyumba ya malamulo.
“Nditha kutsimikiza pano kuti bilu yokhudza zaka sikubwela ku nyumba ya malamulo, komanso kalata (petition )yomwe akuti ikufuna biluyi izakambidwe ku nyumba ya malamulo sikubwelanso ku nyumbaku ndipo izizi zomwe tagwirizana,” iwo anatero.
Bilu yomwe imafuna kupita ku nyumba ya malamulo ngati (private members bill) imaletsa aliyense yemwe ali ndi zaka zodutsa 80 kuyimira nawo pa mpando wa utsogoleri wa dziko.
Koma anthu ambiri anati bilu imeneyi ndiyofuna kulimbana ndi a Peter Mutharika omwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive, ndipo yabwela nthawi yolakwika chifukwa kwangotsala miyezi yochepa kuti tipite ku chisankho chapatatu chomwe chichitike m’dziko muno mu September.
Akunjenjemera eti