
Ntchito yokonza msika wa Kamba munzinda wa Blantyre kukhala wa makono (shopping mall), yayambika ndipo pomwe tinathamangira ku malowa lero Lolemba, tinapeza pamalopa pakudulidwa mitengo kusonyeza chiyambi cha ntchitoyi.
Mbali inayi, anthu omwe amachita malonda awo panja pa msikawu anali akusamutsa katundu wawo kupita naye tsidya la nsewu komwe akuti apatsidwa ndi khonsolo kuti akhale akuyembekezera kaye kwa panopa.
Titafunsa ngati kunsavana komwe kudalipo pakati pa ochita malonda komaso khonsolo ya nzinda wa Blantyre kudathetsedwa, Buka Chaphinza, wapampando wa msikawu wati mbali zonse zokhudzidwa zidakhalirana pansi masiku apitawa komwe zidavetsetsana chimodzi.
“Kukambirana poyambilirapo ndi komwe kudavuta, nkhaniyi ndi yabwino koma chomwe chidavuta, a khonsolo samatiuza bwino bwino. Apapa tauzidwa ndipo ndife okhutitsidwa chifukwa malowa akakonzedwa, ife tidzapezanso mwayi oti tizapange ma bizinezi athu pamenepa,” watelo Chaphinza.
Chaphinza watiuzanso kuti khonsoloyi yawapatsanso malo oyembekezera omwe ali pa mphambano yopita ku chipatala cha Queen Elizabeth. “Atiuzaso kuti amene akufuna kupita ku misika ngati ya Limbe, Zingwangwa, Mbayani komamso pa Chipatala cha Queen Elizabeth, anene akatipezera malo. Izi ndi zomwe takhala tikuwapempha.”
Komabe, m’modzi mwa ochita malonda pa malopa, Emmanuel Somozani wadandaula kuti ngakhale chitukukochi ndi chabwino kwambiri, zodandaulitsa ndi zoti kulumikizana pakati pa iwo ndi khonsolo ya nzindawu sikudayende bwino.
“Ife tikufunadi ndithu kuti msikawu ukonzedwe chitukuko chipite pa tsogolo, chomwe tikungodandaula ife ndi m’mene ndondomekoyi yayendera,” watelo Somozani.
Malingana ndi khonsolo ya nzinda wa Blantyre, pamalopa pamangidwa masitolo amakono komanso malo omwetsera mafuta galimoto. Ntchito yokonza maloyi igwiridwa ndi ndalama zokwana K3 biliyoni.