Nkhani za m’banja zatenga moyo wa AcKim Kajiya m’boma la Thyolo

Advertisement
Malawi24

Apolisi m’boma la Thyolo atsimikiza za imfa ya Ackim Kajiya a zaka 38 omwe adzimangilira ku denga la nyumba yawo kamba ka kusavana ndi mkazi wawo.

M’neneri wa apolisi ya Masambanjati m’bomali, Amos Banda wati Kajiya anapezeka atafa kale pozimangilira pakati pa usiku wa lero.

Malinga ndi Banda ati malemuwa anali pa mkangango ndi mkazi wawo kufikira kuti mkazi yu anafuna kuzipha pomwa makhwala ophera tizilombo koma achibale ndi amene anapulumutsa pomutengera ku chipatala kumene anapeza thandizo la makhwala.

Koma mwamuna wake atamva za nkhaniyi, anaganiza zodzikhweza ku denga la nyumba yake ndipo zotsatira za chipatala zasonyeza kuti Kajiya wataya moyo kamba kobanika.