
Pomwe tangotsala ndi miyezi isanu ndi umodzi kuti tipite ku chisankho chapatatu, m’tsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera wati Mulungu sanalakwitse kumuyika pampando wotsogolera dziko lino. Ndipo sanamuyike kuti alaphere kuyendetsa dziko.
Chakwera analankhura izi kumudzi kwawo ku Kasiya komwe amachititsa msonkhano wa ndale pa Sukulu ya Malembo kwa mfumu yayikulu Khongoni m’boma la Lilongwe.
A Chakwera awuza anthu omwe anasonkhana pamalopa kuti iwowo atumikirabe aMalawi molimbika, ndipo aMalawi asataye chiyembekezo mwa iwo.
Pamsonkhanowu a Chakwera analakhuranso kuti ayamba kuchotsa ntchito nduna zomwe zidzilephera ntchito komanso za chidodo. Koma anthu ena poyankhapo zomwe alakhura a Chakwera, ati m’tsogoleriyu amangodziwa kulakhura koma kuchita kumamuvuta ndipo zokayikitsa kuti akhoza kuchotsa nduna zolephera.
“Nde akuti achotsa nduna zolephera koma tikawona mu kabineti yakeyi nduna zambiri zolephera komanso za chidodo palibe chanzeru zomwe zikupanga,” wina analakhura choncho pa masamba a mchezo.
Ena akuti a Chakwera ayambe kuzichotsa iwowo chifukwa olephera oyambilira ndi iwowo kenako nduna zawozo.