MCP yati mitengo ya zinthu ikukwera kuti ena apeze pochitira ndale

Advertisement
Catherine Gotani Hara

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) yemwenso ndi sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Catherine Gotani Hara, limodzi ndi nduna za zamigodi a Ken Zikhale Ng’oma ati anthu ena akukweza dala mitengo ya katundu mdziko muno ndi cholinga chofuna kupeza pochitira ndale, kuyipitsa boma.

Poyankhula pa msonkhano wa ndale omwe anapangitsa lamulungu masana ku Chibavi mu mzinda wa Mzuzu, sipikala Hara wati iye ngati chipani akuvomeleza za mavuto ambiri amene dziko likudutsamo koma anati anthu ena akubwezeretsa dziko m’mbuyo pofuna kugwiritsa ntchito mitengo ya zinthu ngati chida cha ndale.

M’mawu awo a Zikhale Ng’oma ati anthu ena zikuwapweteka kuti a Lazarus Chakwera akubweretsa ndondomeko zokonzera mavutowa (system), ndipo anati kukweza mitengo ya zinthu ndi ndale zachibwana.

Iwo atsimikizira aMalawi kuti mitengo itsika.

“Ndale zachibwana…kukweza zinthu chifukwa tupita ku zisankho? Chimanga akubisa akufuna zinthu zikwere mtengo,” anatelo a Zikhale Ng’oma.

A Gotani Hara amemezanso anthu kuti adzichita ulimi wa mthilira ponena kuti nyengo sikumapanganika.

Wachiwiri kwa mtsogoleriyu wati nyumba 12, 000 ku Mzuzu zikhale zikulandira ndalama zokwana 70,000 kwacha nyumba iliyonse, ndipo apempha mafumu kuti polemba anthu asalembe mokondera.

Iwo anati kulembana zinthu mokondera zimatukwanitsa boma, ndipo apempha mafumu kuti awonetsetse kuti misika yogulitsila Chimanga simukuchitika chinyengo .