Chakwera athothola nduna za manja lende, akudana ndi chidodo

Advertisement
Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati sasekelera mchitidwe ochedwetsa ntchito ya chitukuko iliyonse mdziko muno ndipo wati adzichotsa nduna zonse zomwe zizigona pa ntchito ndi kuchedwetsa ntchito pamene wati sinzeru kuchita kukakamizana kugwira ntchito.

Poyankhula pa msonkhano wa ndale pa sukulu ya Malembo kwa mfumu yayikulu Khongoni m’boma la Lilongwe lero, a Chakwera ati akudziwa kuti pali ma guru ena a anthu omwe akukhala tchingo kuti ntchito ya chitukuko isayende mothamanga kapena kuti ichedwe, chifukwa choti sakupeza nawo phindu, pamene ati ichi mchifukwa chake ma kontalakitala ena anawaleketsa ntchito.

“Osamangokhala mu ma ofesi kubindikira pa ma computer, koma ati ma documents nkumangosowa koma pa ground popanda chachitika zimenezo ine ayi, wina akamachedwetsa chitukuko ameneyo achotsedwe.” analankhula a Chakwera.

A Chakwera ati si zowona kuti mtsogoleri wa dziko adzikhala otangwanika nkupempha kuti tchito iyende mwachangu pomwe oyendetsa ntchito ali khale, ndipo adzudzula alembi akulu m’maunduna kuti asasekelele mchitidwe ogwira ntchito mwa chidodo pomwe wati osekelera zotele naye achotsedwa nawo limodzi.

“Pali ma director ena amachitira mwano mabwana awo ponena kuti iwo amadziwana ndi a nduna, ati amadziwana ndi a chief of staff ku nyumba ya boma, ati amadziwana ndi advisor wa president, ngakhale ine ndemwe, ati amadziwana ndi a president chibwana cha mtundu umenewo ine ayi, mukamasekelera zimenezo muchotsedwera limodzi,” anatsindika mtsogoleri Chakwera.

A Chakwera anatinso kupezeka kwa mgodi wa Rutile ku Kasiya ndi mwayi kuti dziko litukuke ndipo ati iwo alankhula zambiri akapita ku nyumba ya malamulo posachedwa.

Iwo anati chichokereni 1964 mgodi wa Rutile ku Kasiya wapezeka mu nthawi ino chifukwa Mulungu anabisa cholinga.

Pomaliza a Chakwera atsekulira ntchito yomanga ma sukulu 34 mu mzigawo za maphunziro mdziko muno komwe ana amene akhonza bwino msukulu za primary adzisankhidwira kukachita maphunziro a ku secondary. Iwo ati ntchitoyi iyamba ndi ma sukulu asanu ndi ndalama zochokera ku thumba la boma  la Malawi.