
Pomwe dziko la Malawi likudutsa mu ziphinjo za njala, kusowa kwa mafuta, kusayenda bwino kwa chuma, kuyenda pang’ono pang’ono kwa zitukuko mwa zina, boma lapeza njira ina yogwiritsa ntchito ndalama za misonkho pofokozera aMalawi kudzera ku Hotela ya Golden Peacock momwe Boma likugwilira ntchito mu pologalamu yomwe aMalawi ena ati ndi ya ndale yotchedwa ‘Boma Likutinji’.
Pologamu yomwe yayamba kuwuluka lachisanu sabata latha pomwe kunabwera nduna zinayi a Vera Kamtukule, a Sosten Gwengwe, a Sam Kawale ndi a Vitumbiko Mumba ndipo ikumatsogozedwa ndi nduna yofalitsa nkhani a Moses Kumkuyu lachisanu sabata ino iliponso ku Hotela ya pamwamba ya Golden Peacock mu nzinda wa Lilongwe.
Nduna ya za mafuta ndi Migodi a Ibrahim Matola akhale akuyika kaye pambali zomwe wawalamula wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko a Michael Usi kuti abweretse mafuta m’ma ola 48, ndipo ndunayi ikhale nawo pa pologalamu ya boma likutinji kuyankha zokhudza 52 million litres ya mafuta ya G2G komanso zokhudza magetsi a MAREP.
A Jacob Hara Akhale nawo akukabwerezanso kachingapo zomwe akhala akufotokoza zokhudza misewu ina ya mdziko muno monga M1,M5 , chingeni-Zomba ndi nseu wa Makanjira komanso ndalama zomwe zatoleledwa mu zipata za misewu (tollgate) zomwe bungwe la Roads Fund Administration lidanena kale kuti latolera ndalama zokwana 12.7 billion kwacha chikhazikitsileni zipatazi m’chaka cha 2021.
Anthu ena pa tsamba la Boma (Malawi Government) adzudzula boma posakaza chuma pa zinthu zosayenera pomwe ati kunali kwabwino kuti ndunazi zigwire ntchito molimbika kuti zotsatira zake ndi zomwe zichitire umboni mwa zokha.
Jones Kacheka wati, Boma la a Chakwera likanachitira pologamuyi ku ma office a boma kusiyana ndi kukalipira ma Hotela a pamwamba, ndipo ati uku mkuwononga chuma.
Potsilira ndemanga a Rabson Nyirenda ati boma lazindikira kuti lakanika kuyendetsa bwino zinthu ndipo akungofuna kupaka utoto okongola ku zinthu zowonongeka kale kudzera mnjirayi ndipo ati iyi ndi njira yongodyera misonkho ya aMalawi.
A Lucious Nkhoma ati “Akupatsani 48 hours kuti mubweretse mafuta, go pa ground mukagwire ntchito. Ifeyo zomatiuza kuti boma likutinji nzopanda ntchito chomwe tikufuna ndi ma results ndipo tizaona tokha osachita kutiuza.”
A Emmanuel Nyondo ati; Nchifukwa chani boma likusakaza chuma cha dziko kuchita zomwe ati ndi sewelo.
Pomwe a Chri Christo ati Boma likuchita bwino kubweretsa poyera magwiridwe a ntchito zake pomwe likukwanitsa kuyankha mayankho kwa aMalawi.
Malingana ndi nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu pologalamuyi idzibwera lachisanu ndi cholinga chofuna kuyandikana ndi aMalawi pa m’mene zinthu zikuyendera mdziko muno ndipo sabata latha adati pologamuyi ndi yofunika kwambiri poti aMalawi adzisankha nduna yomwe akufuna kuti ibwere idzalankhule ndi aMalawi.
Boma likuyeneranso kutulutsa ndalama zina lachisanuli kulipira ma allowance a onse oyitanidwa, nthawi ya nyumba zofalitsa nkhani zomwe zifalitse uthengawu, malo ochitila nsonkhanowu, mwa zina.