
Anthu ochita malonda ogulitsa tomato mu msika waukulu mu mzinda wa Blantyre adandaula kamba ka kukwera kwa mitengo yowodera tomato zimene zikuchititsa kuti bizinezi yawo ilowe pansi.
Modzi mwa anthu ochita malondawa, Christopher Gama wati tomato akumaoda K220,000 pa Dishi (bikili ya ma litazi 20) kusiyana ndi nthawi zonse pamene amaoda K15,000. Izi zachititsa kuti nawo azikweza mitengo kuti apeze phindu.
“Ndikugulitsa tomato mutatu K2,000 wina k3,000 kuti mwina tipeze mpindu koma izi zikuchitsa kuti malonda anthu asayende pa msika ndipo wambiri akumaonongeka kusowa ogula,” kuyankhula kwa Gama.
Iye anapitiriza kupempha boma kuti liyambe kugawa zipangizo za ulimi kwa alimi olima mbeu za kudimba mu nthawi yoyenerela ngati njira imodzi yothana ndi vutoli.
Mayi ena omwe anati tisawatchure dzina adandaula kamba ka chitonzo komaso kuyankhulidwa mawu achipongwe ndi anthu ogula.
Mai wa anati “Tomato wambiri akumachokera ku Zambia wina ku mpoto, chifukwa cha kukwera kwa ma thilasipoti, tikugula modula kwambiri zimene zikutikakamiza ifeso kukweza mitengo.”
Tsamba lino lapeza kuti chaka chino alimi ambiri sanalime tomato mu nthawi yake kamba ka kukwera kwa mitengo ya zipangizo za ulimi komaso dzuwa limene linakhudza m’dera ambiri m’dziko muno.