
Bungwe lomenyera ufulu wa anthu a ulumali la Federation of Disability organizations in Malawi (FEDOMA) lati anthu ambiri a ulumali m’dziko muno makamaka amayi ndi atsikana amakanika kukanena kwa adindo za nkhanza zomwe akukumana nazo.
Malingana ndi m’modzi mwa akuluakulu ku bungweli, a Ethel Kachala, mchitidwewu ndi osakhala bwino chifukwa umakolezera nkhanza kwa anthu a ulumali.
A Kachala anati ndi zodandaulitsa kuti anthu ambiri a ulumali akukumana ndi mavuto adzaoneni monga kusalidwa koma iwo eni amamangika kuika izi pambalambanda.
“Kwa nthawi yaitali, anthu a ulumali m’dziko muno akhala akuchitilidwa nkhanza zosiyanasiyana koma anthuwa amasankha kukhala chete chifukwa cha mantha,” anatero a Kachala.
Iwo anatsindika kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wachibadwidwe posatengera kuti ali ndi ulumali kapena ai.Iwo anapitiliza kumema anthu onse a ulumali kuti azimasuka ndi kufotokozera adindo osiyanasiyana za nkhanza zomwe akukumana nazo.
A Kachala anadandaulanso kuti anthu ambiri a ulumali amapangilidwa ziganizo zokhudza moyo wawo ndi anthu ena zomwe akuti sizimapeleka mpata kuti anthu a ulumali afotokoze zosowa zawo.
“Ndi khumbo lathu kuti anthu a ulumali m’dziko muno azikhala nawo m’maudindo osiyanasiyana opanga ziganizo kuti azitha kupanga nawo ziganizo zokomera iwo,” anafotokoza a Kachala.
Pakadalipano, bungweli lakhazikitsa ndondomeko ya ntchito yomwe igwilidwe kwa zaka ziwiri m’maboma a Balaka, Kasungu, Ntcheu komanso Zomba pofuna kulimbikitsa anthu a ulumali kuti azitha kukhala nawo m’maudindo opanga ziganizo.
Mwa zina, mu ntchitoyi, bungwe la FEDOMA liphunzitsa anthu a ulumali pa nkhani zosiyanasiyana zokhudza maufulu awo komanso kukhazikitsa ma komiti a anthu a ulumali m’madera osiyanasiyana pofuna kuthana ndi nkhanza zomwe anthu a ulumali amakumana nazo.
Ndipo m’mawu ake, mkulu oyang’anira achikulire komanso anthu a ulumali ku khonsolo ya Balaka a Stanley Chisi anati ali ndi chikhulupiliro kuti ntchitoyi ithandizira kwambiri kuchepetsa mavuto omwe anthu a ulumali amakumana nawo m’bomali.
A Chisi anati pakadalipano, ofesi yawo ikukanika kugwira bwino ntchito zake kaamba ka kusowa kwa ndalama komanso zipangizo.
Bungwe la FEDOMA ligwira ntchitoyi ndi thandizo la ndalama lochokera ku bungwe la Bread for the World la m’dziko la Germany.