A Polisi apa msewu anyanya – Christopher Chiomba

Advertisement
Chiomba

Yemwe akufuna kudzapikisana nawo ngati mtsogoleri wa dziko lino pa zisankho zomwe zichitike mwezi wa September pa 16, Christopher Mike Chiomba a chipani cha Nzika Coalition ati ulendo wina anakumana ndi a polisi apa msewu mmalo oposera makumi atatu ndi asanu (35) kuchokera ku Lilongwe kupita ku Blantyre.

A Chiomba anayankhula izi lachiwiri pa wayilesi ya kanema ya Zodiak pomwe amacheza ndi Leah Malekano.

Ngakhale kuti anafotokoza nkhani zambiri koma choyambilira anati nawonso akhuzidwa ndi kusayenda kwa zinthu komwe kwakuta dziko lino.

Iwowa ndi m’modzi mwa anthu omwe amapanga malonda amayendedwe maka kunyamula katundu kuchokera mmayiko akunja ndinso m’dziko mommuno pogwiritsa ntchito galimoto zikuluzikulu (Truck).

Mwamavuto ena anati padakali pano kuti abweretse katundu kuchokera mayiko akunja pakumakhala zotsamwitsa zingapo muzipata mwathumu zomwe zikumawachedwetsa.

Komanso anatsindika zomwe zimawakhumudwitsa kwambiri pa msewu monga kuchuluka kwa malo oposa 35 omwe apolisi apa msewu amayima zomwe mbali ina zimachedwetsa kagwiridwe kawo ka ntchito.

“Ma truck ena amakhala anyamula katundu olingana ndi nthawi nde akamongoyimisidwa ndi a polisi-wa nde kuti amakhala akutaya nthawi,”anatero a Chiomba.

Anapitilira kufotokoza kuti sitingakambe za chuma cha dziko opanda nthawi ndipo apolisi pa msewu anyanya.

Poyankhapo funso lokuti : simufuna apolisi apa msewu azikuyimisani?

iwo anati,”Pali nkhani ya Chitetezo cha dziko ndiye pali nkhani ya zifukwa zawo zimene apolisi amayimira munsewu komanso apolisi ochuluka amagwiritsa ntchito galimoto zawo zakunyumba.”

Mwachitsanzo anati akakuyimitsa ndipo akakupeza ndi mulandu amakulozera kuti ukalipire mulandu wakowo pa galimoto yomwe siya polisi koma yawo ya kunyumba.

“Ine ndimadabwa kuti tikalipire milandu pa galimoto yawo (Civilian vehicle) Insurance yake itiyo?”anafunsa Chiomba.