Anthu asandusa sukulu ya Chiwoko ngati malo ochitira za chisembwere

Advertisement
Chiwoko Primary School - Lilongwe

Komiti yoyang’anira sukulu ya Chiwoko mu mzinda wa Lilongwe adandaula chifukwa chakuchuluka kwa mchitidwe wogwiritsa ntchito zipinda zophunzilira ana ngati malo ochitira za dama.

Poyankhula pa msonkhanowu wa makolo omwe udachitika loweruka lapitali, komiti ya sukuluyi idati pali abambo ena omwe akumatengana ndi azimayi ndikumagwiritsa ma kalasi pochita zachisembwere.

Iwo ati nawonso achinyamata adapezerapo mwayi ndikumagwiritsa ntchito makalasiwa pogonana.

Izi zakhumudwitsa akuluakulu a pa sukuluyi ndipo apempha anthu ozungulira sukuluyi kuti asiiretu mchitidwewu.

“Tilemba alonda oyang’anira zipinda zomwe anthuwa amagwiritsa ntchito kuti azawagwire ndikuchitisidwa manyazi”, adatero mmodzi mwa akuluakuluwa.

Iwo adaonjezera kuti zimakhala zomvetsa chisoni kupeza makondomu ogwiritsa ntchito kale mzipinda zophunzilira zomwe zimasokoneza ntchito ya ukhondo pa sukuluyi.

Komiti yoyendetsa sukuluyi inadandaulanso kuti mabanja ena akumalowa mkati mwa sukuluyi ndikumagwiritsa ntchito zimbuzi za sukuluyi zomwe zikupangitsa kuti ukhondo ukhale ochepa.

Iwo ati pali chiopsyezo choti ana akhoza kutenga matenda ngati mchitidwewu siutha.

Poyankha, makolo adapempha sukuluyi kuti ikhwimitse chitetezo ndicholinga choti ana awo asatenge matenda kusukuluyi.

Zina mwa nkhani zomwe anakambirana ndi makolo ndi yokhuza kupeza njira yopezera ndalama yokonzetsera zipinda zophunzilira zomwe zimadontha nthawi ya mvula.

Apa, makolo adagwirizana kuti mwana aliyense azisonkha K1, 000 pa mwezi mpaka mwezi wa September kuti akonze ma buloko anayi.