
Phungu wa dera la kumpoto m’boma la Balaka a Tony Ngalande wapeleka ndamala ya ngongole yokwana 24 miliyoni kwacha ku magulu achinyamata, amai komanso abambo ati pofuna kutukula ntchito za malonda zing’onozing’ono.
A Ngalande omwenso awonetsa chidwi chodzapikisana nawo pa mpandowu mu dera lomwe langokhazikitsidwa kumene la Balaka Ngwangwa ati ntchito za malonda zing’onozing’ono zimathandizira kukweza chuma cha dziko lino.
Iwo amayankhula izi Loweluka pamene amapeleka ndalamayi kwa magulu okwana 60. Iwo anati amalonda ang’onoang’ono amakumana ndi mavuto osiyanasiyana zomwe zimalepheretsa malonda awo kutukuka.
“Ndikudziwa kuti ochita malonda ngati a mizimbe, mandasi komanso masamba mipamba yawo imakhala yochepa kwambiri.Choncho ndinaona kuti ndi kofunikira kwambiri kuti amalonda amenewa ndiwathandizile ndi mwayi wa ngongole.
“Ndikukhulupilira kuti ndalamayi ithandizira kwambiri kutukula ma bizinesi awo komanso miyoyo yawo,” adatero a Ngalande.
Malingana ndi phunguyu, gulu lililonse lalandira ndalama yokwana K400,000.Maguluwa ndi a achinyamata, amai komanso abambo.
Mai Maria Henderson omwe ndi wapampando wa gulu la amai lotchedwa Chisomo athokoza phunguyi powapatsa ngongoleyi zomwe ati zithandizira kutukula bizinesi yawo.
“Nthawi zambiri, zimakhala zovuta kwambiri kwa ife a bizinesi zing’onozing’ono kuti tipeze mwayi wa ngongole.Mwachitsanzo,timasowa chikole chomwe mabungwe obweleketsa ngongole ambiri amafuna kuti tiwonetse asanatipatse ngongoleyo,” adatero mayi Henderson.
Pa mwambowu panafika anthu osiyanasiyana omwe ndi kuphatikizapo atsogoleri a zipembedzo komanso mafumu.