
Bambo wina, Yamikani Kawala wa zaka 28, yemwe amachita malonda ogulitsa makala, wamwalira atadumphira mu mtsinje pofuna kuthawa a chitetezo a nkhalango atakumanizana naye ali ndi matumba awiri a makala.
Malinga ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe a Khumbo Sanyiwa, izi zidachitika pafupi ndi nkhalango ya Dzalanyama Forest Reserve pa 31 mwezi watha cha ma 4 koloko masana.
Mkuluyo adali pa njinga ya kapalasa atanyamula makala omwe adagula mu nkhalangoyo, ndipo atangooloka mtsinjewo kufika m’mudzi wa Wilson adakumana ndi a chitetezo.
Bamboyu atawona achitetezo adaganiza zosiya njingayo ndi kudumphira mu mtsinje kuti athawe posambira kukafika tsidya lina.
“Koma mwachisoni sadakwanitse kutero, ndipo adamira. Thupi lake lidapezeka likuyandama tsiku lotsatira,” atero a Sanyiwa.
Zoyeza za chipatala zidapeza kuti a Kawala, omwe amachokera m’mudzi wa Chongo mfumu yaikulu Chiseka ku Lilongwe konko, adamwalira kaamba kolephera kupuma.