Chonde chonde kwezani mtengo wa mafuta – apempha choncho a Kapito a CAMA

Advertisement
Malawi

Akayamba kupezeka bwino tikweza – a Kachaje

Iyi ya mafuta sichoka m’bwalo. Mkulu amene amamenyera ufulu wanu anthu ogula malonda a John Kapito achondelera ku boma kuti akweze mtengo wa mafuta a galimoto. Iwo anena izi pamene dziko lino likukumana ndi vuto la kusowa kwa mafuta.

Malinga ndi nyuzipepala ya Times, a Kapito ati njira imodzi yothana ndi kusowa mafuta komanso kupezeka kwake ndi anthu a chinyengo ndi kuwakweza mtengo mafutawo basi. Iwo amanena izi pamene apolisi akhala akunjata anthu ena ati kamba kogulitsa mafuta mwachinyengo.

“Amanga anthu mpaka liti? Pakufunika njira yothana ndi vutoli, imodzi mwa iyo ndiko kukweza mtengo mafuta,” a Kapito akuti anatero.

Mmbuyomu a Kapito adapemphanso boma kuti livomereze kuti bungwe loyang’anira za madzi la Blantyre Water Board livomerezedwe kukweza mtengo wa madzi ake.

Kukwera mtengo kwa mafuta mu dziko lino kwakhala kuli mkamwamkamwa ngakhale zikuoneka kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera akuchita jenkha poopa kuti ziwaipitsira tsogolo lawo, maka pano pamene nkhani zachuma zikukhala ngati zawavuta.

Pachisanu, a Henry Kachaje a bungwe la MERA nawo adauza a phungu a nyumba ya malamulo kuti aunikira bwino zokweza mitengo ya mafuta ati chifukwa kuonetsetsa kuti mafuta afike mu dziko muno kukuvuta ndipo kukufuna ndalama zambiri.

Iwo adanena kuti nyengo zowawa zomwe dziko lino likudutsa mu nthawi ino pomwe akupeza mafuta ndi owerengeka zikatha, aunika kuti akweze mitengo ya mafuta.

Malinga ndi kafukufuku, Malawi ndi lachinayi mu Africa muno kukhala ndi mafuta wokwera mtengo kwambiri. Izi zili chomwechi ngakhale kuti anthu ochepa okha ndi amene amalandira ndalama zochulukirapo.