Anjatidwa kamba kopha aMalume ake

Advertisement
Dedza police

A Polisi m’boma la Dedza amanga mnyamata wa zaka 20, Joseph Sankhani pomuganizira kuti wapha a malume ake.

Malinga ndi m’neneri wa Polisi ya Dedza, a Beatrice Jefita ati mnyamatayu yemwe amachokera m’mudzi mwa Kawaliza, mfumu yayikulu Kasumbu m’bomalo anapha a malume ake a Chewile Banda pa usiku wa 11 January, 2025 ku nkhalango ya Chingoni.

A Jefita anati patsikulo mnyamatayu ndi aMalume ake anagwirizana zopita ku nkhalango ya Chongoni kuti akabe mitengo, ndipo atafika kumeneko Sankhani anawatema aMalume ake kumutu ndi chikwanje.

“Atawapha a malume ake anawachotsa ziwalo monga maso, mano ndi lilime, kenako anasiya thupi la malume akewo pakati pa nkhalango yo,” anatero a Jefita.

Malinga ndi a Jefita, mnyamatayu anatenga ziwalozo kupita nazo kwa munthu wina ochita malonda m’bomalo kuti amugule, ndipo munthuyu ndiyemwe anatsina khutu aPolisi omwe anakwanitsa kumugwira mnyamatayu.

Pakalipano thupi la malemewa lili pachipatala cha Dedza komwe akudikira kuti aliyeze.