Ndili ndi kuthekera kotsogolera chipani cha UTM – Kambala

Advertisement
UTM

M’modzi mwa yemwe akufuna kupikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM), a Newtwon Kambala lero apereka zikalata zowonetsa chidwi chofuna kupikisana nawo ku msonkhano waukulu omwe ukhale pa 17 November, 2024 mu mzinda wa Mzuzu.

Polankhula atapereka zikalatazi, a Kambala anati Iwo ali ndi kuthekera kotsogolera chipani cha UTM Ku zisankho zomwe zikubwela chaka cha mawa.Malinga ndi a Kambala, cholinga chawo popikisana nawo pa udindowu, ndikufuna kukwaniritsa masomphenya omwe a Saulos Chilima anali nawo ofuna kusintha miyoyo ya a Malawi.

“Ndili nacho chitsimikizo kuti ndidzapambana pa udindowu. Ndipempheso mthumwi zimene zidzakhale ndikuthekera kovota kuti adzasankhe mosamala, ndipo asakomedwe ndi ndalama,” Iwo anatero.

Iwo anatsindika kuti chipani cha UTM sichili pa msika ndipo sichikugulitsidwa kamba kakuti ndi chipani chokhacho chomwe chingasithe miyoyo ya a Malawi.

Anthu ena otsatira chipani cha UTM omwe ali pambuyo pa a Kambala anawaperekeza kuchokera pa area 18 Memorial tower mpaka kukafika ku likulu la chipanichi ku area 10 komwe anakapeleka zikalatazi.Ena mwa a kulu akulu a chipani omwe anaperekeza a Kambala ndi a Chidanti Malunga ndi Mayi Annie Makuta.

Anthu omwe apereka zikalata zawo padakalipano ndi a Dalitso Kabambe, a Mathews Mtumbuka, Mayi Patricia Kaliati komanso a Newton Kambala omwe apereka lero. Onsewa akufuna kutenga utsogoleri wa chipanichi.

Advertisement