Mzimba Queens ndi akatswiri a Salima Sugar Netball Tournament

Advertisement
Mzimba

Timu ya mpira wa manja ya Mzimba Queens yakhala akatswiri a Salima Sugar Netball Tournament chigawo cha kumwera kwa boma la Mzimba.

Timu Mzimba Queens yathambitsa  timu ya Raiply Queens ndi mitanga yokwana 56 – 44. Timu ya Mzimba Queens kuti ifike mundime  yotsilidzayi inagonjetsa timu ya Mzimba Police. Pomwe mundime ya chipulura inagonjetsa matimu a Young queens, Topic Sisters, Unique Sisters, Hotlions ndi Makulande.

Mphunzitsi watimu ya Mzimba Queens Patricia Vandekha Chunga wauza Malawi24 kuti iye ndiokondwa kuti timu yake yakhala akatswiri achikho chimenechi ku chigawo cha kumwera kwa Mzimba.

“Ndine okondwa kuti tapambana komanso ndivomeleze kuti timu ya Raiply inatipatsa game yabwino kwambiri, pomwe tikupita chitsogolo taona mavuto athu ndipo tikonza kuti mundime tikupitayi tikachite bwino,” watero Chunga.

Akatswiriwa alandira ndalama zokwana K300,000, ndi chikho,  Raiply Queens ya pasidwa K200,000 pamene Mzimba Police yalandira K150,000 ndipo timu ya Unique Sisters yalandira K100,000.

M’mene zateremu timu ya Mzimba  Queens ndiyomwe ikaimire chigawo chakumwera kwa Mzimba pa masewero omwe achitike mwezi wa mawa chigawo chonse chakumpoto.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.