Osatigulitsira Chilumba chathu – Mpingo wa Anglican wauza Boma

Advertisement
Likoma Island

Mpingo wa Anglican wauza Boma la Malawi kudzera ku unduna wa Zokopa alendo kuti zilumba za Likoma, Chizumulu komanso Mbamba sizili pamsika, ndipo zilumba zimenezi ndi za anthu omwe akukhalapo.

Malinga ndi chikalata chomwe watulutsa Mpingowu chomwe chasayinidwa ndi RV. Fanuel Magangani, chitukuko chilichonse chomwe chifuna kupangika pa zilumba zi chizikhudza anthu okhala pompo kuti nawonso azipindula.

“Aliyense ofuna kuchita Malonda pa Likoma azitipeza ife ndi anthu okhala pamalopa ndikunva madandaulo athu, kumva zomwe tikufuna, komanso kulemekeza chikhalidwe chathu,” iwo anatero.

A Magangani anenetsa kuti Chilumba cha Likoma sichikugulitsidwa ndipo palibe aliyense abwere kuchoka kunja kuti akatenge Malowa.

“Malowa ndi a anthu omwe amakhala pamalopa ndipo chilichonse chomwe Boma likufuna kupanga liziwadziwitsa anthuwa osati agati anthu wamba koma kuwadziwitsa ngati anuwake a Malowa ,” anatero a Magangani.

Chikalata cha Mpingowu chikudza pomwe panali mphekesera kuti Boma likufuna kugulitsa Chilumba cha Likoma kwa namakhumutcha wina wakunja.

Masiku apitawo Boma nalo linatulutsa chikalata kunenetsa kuti sakugulitsa Chilumba chi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.