Sitikugulitsa Chilumba cha Likoma, Boma lakana

Advertisement
Likoma Island

Boma la Malawi kudzera ku unduna wa Zokopa Alendo lakanitsitsa kuti lilibe maganizo ogulitsa Chilumba cha Likoma, komanso kusamutsa anthu omwe amakhala pamalopa.

Malingana ndi chikalata chomwe chasayinidwa ndi Mlembi wamkulu ku unduna wa Zokopa Alendo, a Chancy Simwaka, zomwe zinalembedwa mu nyuzipepala ya Malawi News pa 14 ndi pa 20 September komanso pa 21 ndi pa 27 September kuti boma la Malawi likugulitsa Malowa ndi zabodza.

“Boma la Malawi lilibe mgwirizano uliwonse ndi munthu aliyense ofuna kuchita malonda kuno pa zokhudza Chilumba cha Likoma. Ndipo ife ngati unduna wa Zokopa Alendo tikutsimikizira a Malawi Kuti Chilumba cha Likoma sichikugulitsidwa ndipo sichidzagulitsidwa,” atero aSimwaka.

A Simwaka ati boma lipitiliza kukumana ndi anthu omwe akufuna kumapanga za Malonda pa malo osiyanasiyana okopa anthu monga Likoma Activity Centre Project, ndipo aziwonetsetsa kuti mgwirizano uliwonse ochita malondawa ndi ovomelezeka komanso opindulira a Malawi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.