Kuchotsa mimba kwakula ku Mzimba

Advertisement
Mzimba

Achinyamata m’boma la Mzimba akhudzidwa ndi chiwelengero chokwera cha matenda opatsirana pogonana komanso nkhani zochotsa mimba mwachisawawa pakati pawo ponena kuti izi zikusokoneza maphunziro awo. 

Izi zanenedwa pomwe bungwe la Mzimba Youth Organisation, mothandizidwa ndi bungwe la UNICEF, kudzera mu bungwe la achinyamata la National Youth Council, lidakonza m’kumano wokambirana pakati pa achinyamatawa ndi ogwira ntchito m’bomalo. 

Glory Chilinga kuchora ku Mzimba Inspired Youth Talent Club wati izi zachitika chifukwa chakusowa chinsinsi pa chipatala cha bomali zomwe zimapangitsa achinyamata kulephera kupeza njira zolerera ndi mankhwala ena chifukwa chowopa kulembedwa kuti ndi adama.

Mzimba
Chilinga: Zipatala zathu zilibe chinsisi.

M’mawu ake, wachiwiri kwa mkulu woyang’anira ntchito za umoyo wa achinyamata pa chipatala cha m’bomalo, Toously Kondowe, wagwirizana ndi Chilinga ponena kuti mpoyenera kukhazikitsa ngodya zakuti achinyamata pa chipatalachi adzitha kupeza thandizo mosaopa komanso mosungilidwa chinsisi.

Mkulu wa bungwe la Mzimba Youth Organization (MYO), Moses Nkhana, wati adindo adzitsatira zomwe achinyamatawo anena kuti kuti awonenetsetse kuti zachitika.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.