Musadule mtengo opanda chilolezo cha Khonsolo – ZCC

Advertisement
Tree

Khonsolo ya mzinda wa Zomba (ZCC) yati anthu a mzindawu siololedwa kudula mtengo uliwonse kaya uli pakhomo pawo kapena ayi, popanda chilorezo cha Khonsoloyi.

Malingana ndi zomwe Khonsoloyi yasindikiza pa tsamba lake la mchezo la Facebook, aliyense ofuna kudula mtengo akuyenera kulembera kalata kwa mkulu wa Khonsoloyi kupereka zifukwa zomveka bwino paganizo lodula mtengo mzindawu.

“Chonde tsatirani ndondomeko izi pankhani ya mitengo, lembani kalata kwa mkulu wa khonsolo ya Mzinda wa Zomba ndipo oyang’anira chilengedwe ku Khonsolo ya Mzinda wa Zomba adzabwera nkudzaona ndi kutsimikiza zifukwa zomwe mukufuna kudulira mtengowo,” yatero Khonsoloyi.

Nkhonsoloyi yaonjezera kunena kuti ngati Khonsoloyi yavomereza kuti mtengo udulidwe, padzakhala kuunikila ngati mtengowo udulidwe ndi anthu a ku Khonsoloyi kapena ngati munthu adule yekha.

Khonsoloyi yati okhawo omwe adzaloledwe kudula mtengo adzakhala kuti apeleka zifukwa zokwanila zodulira mtengowo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.