Chipwilikiti chidabuka kunyumba yachisoni ku Zomba

Advertisement
Police

Chipwilikiti chidabuka kunyumba yachisoni pachipatala chachikulu cha Zomba pomwe achibale amatenga thupi la dalaiva yemwe adawomberedwa Lamulungu ndi apolisi ku 4 miles mu mzindawu.

Ma dalaiva komanso anzake amalemuyi adatseka nsewu opita ku Blantyre pafupi ndinyumba yachisoniyi ndipo adawotcha matayala komanso samalola kuti galimoto zizidutsa pamalowa ati posonyeza mkwiyo waeo pazomwe adachita apolisiwo powombera ndikupha nzawoyo.

Nkhope zidali zachisoni pomwe thupi lamalemu Zakeyu Matekenya limachoka panyumba yachisoni yapa Chipatala chachikulu cha Zomba ndipo anthu adaperekeza galimoto yomwe idanyamula malirowa kukafika mu mzinda wa Zomba akuyenda pansi uku akuyimba nyimbo zachisoni.

Poyankhula ndi Malawi24, wapampando wama dalaiva m’chigawo chaku mmawa Harry Manjawira wazuzula zomwe adachita apolisi powombera nzawoyo.

Manjawira wati akuyembekezera pamodzi ndi achibale amalemuyi kuti adzakambirane zatsogolo lankhaniyo popeza Malemu Zakeyu wasiya mkazi ndi mwana osakwana chaka chimodzi 

Iye wathokoza apolisi chifukwa chopereka chithandizo cha bokosi, zakudya komanso galimoto yomwe yatenga anthu opita kumaliro Boma la Phalombe.

Malemuwa adawomberedwa Lamulungu pa 4 Miles Roadblock ndi apolisi chifukwa ati sadayime pantjawi yomwe amamuyimisa.

Thupi la malemuwa lalowa m’manda m’boma la Phalombe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.