Timu ya Baka City yalandira ubatizo wa zigoli 

Advertisement
Baka City

Matimu omwe sadzaiwala Mighty Mukuru Wanderers mu chaka cha masewero a mpira cha 2024 afika pa awiri tsopano.

Matimu onsewa ndi akuchigawo cha kumpoto kwa dziko lino ndipo ndi a Baka city komanso Mzuzu city Hammers omwe afwafwanthidwa ndi zigoli zokwana 18 mumasewero awiri okha.

Mwezi wa August, Nyerere zinakokera kuwuna Ma Hammers ochokera mu mzinda wa Mzuzu ndi zigoli zokwana 8 kwachilowere, ndipo paja amati linda madzi apite ndiye udziti ndadala, akanadziwa anyamata a Baka city sakanaponda pa bwalo la Kamuzu kamba koti lero pa masanawa, Nyerere sizinamvere chisoni m’mene Baka city ikudwalira mu League pamene zakwanitsa kuifwafwantha ndi zigoli 10 Kwa chilowere.

Isaac Kaliati, Clement Nyondo, Gadie Chirwa ndi ena mwa anyamata amene anatenga gawo lalikuru potafuna Baka city komanso kupangitsa kuti Ma minibus opita ku Bangwe atsike mtengo kutsatira chipambanochi.

Pakadali pano, Manoma ali pa nambala yachiwiri pa mndandanda wa ma team 16 amene ali mu ligiyi pamene ali ndi ma points okwana 41 atasewera masewero 20. Ndipo timu ya Silver Strikers ikadali pa mwamba ndi mapointi 45 ndipo yasewera masewero okwana 19.

Ku Mzuzu, ma team a Moyale Barracks ndi Creck Sporting alepherana posagoletsana chigoli chilichonse.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.