Apolisi apha dalaiva ku Zomba

Advertisement
Zomba

Chipwilikiti chabuka ku 4 miles mu mzinda wa Zomba potsatira kuphedwa kwa dalaivala wina ndi apolisi.

Pakadali pano, anthu okwiya agendana ndi apolisi ndipo nsewu wa Zomba kupita ku Blantyre awutseka.

Mphekesera zikumveka kuti wapolisi yemwe wawombera dalaivalayo nayenso waphedwa ndi anthu olusa.

Thupi la dailavayo, yemwe dzina lake ndi Zakeyu Matekenya, akulisunga kunyumba yachisoni pachipatala chachikulu cha Zomba kuyembekeza kuti alipime.

Poyankhula ndi Malawi24, bambo ake amalemuwa a Gedion Matekenya ati ali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha ifa ya mwana wawo yemwe adati ndimwana yekhayo yemwe amawathandiza pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Iwo ati akudikilira kuti amve kuchokera kwa apolisi kuti awauze chomwe chachitika kuti mwana wao awomberedwe.

Poyankhulanso, mmodzi mwa akulu akulu abungwe la madalaivala m’dziko muno a Booster Itika adzudzula zomwe achita apolisiwa.

Iwo ati ngati dalaiva adalakwitsa malamulo a pansewu, padali njira zomwe apolisi akadatsatira osati kumuwombera.

Thupi lamalemu Zakeyu Matekenya likalowa m’manda Lolemba ku mudzi kwawo kwa Matepwe, Mfumu yayikulu Kaduya, m’boma la Phalombe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.