Anthu achikulire ayamba kulandira 18,000 kwacha pamwezi kuchokera Ku Boma

Advertisement
Sendeza

Boma, Kudzera ku unduna owona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa mayi ndi abambo, lanena kuti anthu achikulire m’dziko muno ayamba kulandira ndalama yokwana K18,000 pamwezi kuti idziwathandiza pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Anena izi ndi Jean Sendeza omwe ndi nduna yowona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ku nyumba ya malamulo Lachinayi.

A Sendeza anati ndondomeko yi iyamba chaka cha mawa.

Iwo ati boma liyamba kaye ndi achikulire okwana 166,000 mu ndondomekoyi isanafikire achikulire onse mdziko muno.

“Ngati unduna, mu lamulo limeneli kuyambira ndime 1 mpaka 17 tinayika ndondomeko yoti azathu achikulile ayambe kumalandirako kenakake kangachepe kotereku mu ndondomeko yathu tinakonza kuti anthu okwana 166,000 achikulire akhale akulandira kangachepe Kuti kazitha kuwathandiza pamene akukhala makuka mwawo,” iwo anatero.

Ndunayi inapemphaso anthu m’dziko muno kuti asiye kuchitira nkhanza a chikulire ndipo agwirane nanja powasamalira anthu a chikulire wa.

“Chomwe ndingapemphe Kwa azanthu andale , amipingo, a mabungwe ndi aliyense tiyeni tigwilane manja kupeleka uthenga kuti kuzunza achikulire mkosayenera, achikulire tiatenge ngati makolo athu komanso aliyense amene mumamudziwa kuti ndi m’bale wathu,” anatero a Sendeza.

A sendeza anawuzaso nyumbayi kuti kuchoka mwezi wa January chaka chino kufikira pano, achikulire okwana 18 ndi omwe aphedwa, yomwe ndi nambala yayikulu kwambiri.

“Kotero ngati unduna tinabweletsa lamulo mu nyumba ya Malamulo imene aphungu analikambilana ndi kulivomereza, ndipo nawo a President analivomeleza Kuti ndi lamulo lofunikira. Pamene tukamba pano lamuloli layamba kugwira ntchito pa 16 mwezi uno, ndipo aliyense azipezeka akuzunza azanthu achikulire ameneyo azilandira chilango choyenerera,” anatero a Sendeza.

Dzulo aphungu ambiri akunyumba yamalamulo anaonetsa nkhawa pakukula kwa mchitidwe wankhaza zochitira achikukire.

Polakhulapo, Phungu wa dera la Zomba Lisanjala a Susuwele Banda, anati ndi zokhudza kwambiri ndi mene anthu akuwapangira nkhanza achikulire, kuwanyoza komanso kuwanena kuti ndi afiti.

Iwo anapitiliza kunena kuti ngati dziko ndi koyenera tiziwasamalira azanthu achikulire wa osati kuwapangira nkhanza.

A Banda anayamikira Boma chifukwa choyamba kuwapatsa anthu achikulire ndalama yoti azithandizikira pa moyo wawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.