Agamulidwa kukakhala kundende kamba kobela anthu mu dzina la NEEF

Advertisement
Balaka

Bwalo la milandu la Ulongwe Magistrate m’boma la Balaka lagamula bambo Anack James kuti akakhale kundende kwa chaka chimodzi ndi theka, komwe akagwire ukaidi wakalavula gaga kamba kobela anthu ndalama mu dzina la bungwe lobwereketsa ndalama la National Economic Empowerment Fund (NEEF).

Malingana ndi zimene bungwe la NEEF latsindikiza pa tsamba lake la mchezo, a James adaba ndalama zokwana MK140,000.00 kugulu la anthu asanu ndi awiri omwe aliyese anapeleka ndalama zokwana MK20,000.00 ngati chikole powalonjeza kuti apeza mwayi wangongole ku bungweli.

Gulu la anthu omwe adaberedwawa linapangidwa kuchokera m’mudzi mwa Chigwenembe, T/A Amidu, m’boma la Balaka pofuna kuthandizidwa ngongole gakhale oganizilidwayu samagwira ntchito ku bungwe la NEEF ndipo cholinga chawo chinali kubela anthuwa.

“Chomwe chinatsitsa dzaye kuti njovu itchoke mnyanga n’chakuti bambo James anauza mai Angella Banda omwe anali membala wagululi komanso mboni yoyamba kukhoti kuti atumize ndalama yomwe anasonkha ngati guluyi kwa agent kuti iwo atenge.

“Koma agent atawona izi anayamba kukaikila popeza mai Angella amawadziwa ndipo anakatsina khutu apolisi za nkhaniyi. Apa ndipomwe bambowa anagwidwila ndikukatsekeledwa mchitokosi ku police ya Ulongwe,” latsindika motero bungwe la NEEF. 

Ndipo popeleka chigamula chake, Second Grade Magistrate, Peter Mkuzi anagwilitsa ntchito gawo 99, ndime yoyamba la malamulo adziko lino lomwe limakamba zakunamiza anthu ngati ogwila ntchito m’boma kapena nthambi zaboma ndicholinga chofuna kuwabela ndipo ochita izi amayenera kulandila chilango chokhwima chokakhala kundende kwa zaka khumi komanso kukagwira ntchito yakalavula gaga.

Atawunikila mbali zina za nkhaniyi, Magistrate Mkuzi anagamula bambo James kukakhala kundende kwachaka chimodzi ndi theka ndinso kukagwila ntchito yakalavula gaga.

A James amachokera mmudzi mwa Chikanda, T/A Mwambo m’boma la Zomba.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.