Tili pa mavuto chifukwa atsogoleri sakudziwa chochita – Kabambe

Advertisement
Former Reserve Bank of Malawi governor Dalitso Kabambe

Yemwe anali gavanala wa banki yayikulu ya Reserve a Dalitso Kabambe, wati dziko la Malawi likudutsa m’mavuto adzaoneni chifukwa choti linasankha ndikuyika anthu m’maudindo omwe sakudziwa choyenera kuchita.   

Kabambe yemwe ndi m’modzi mwa anthu omwe akukapikisana nawo paudindo wa mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM), wanena izi pomwe amayankhula ndi wayilesi ya Times mu pologalamu yapadera yomwe yawulutsidwa Loweluka.

Iye wati mtsogoleri amayenera kukhala wamachawi, wodziwa choyenera kuchita nthawi zonse zomwe wati sizikuchitika pano. Iye wati izi zapangitsa kuti chuma cha dziko la Malawi chisokonekere, ndipo wati, “Aliyese pano m’dziko muno akungolira mayomayo.”

“Vuto lathu lalikulu ndi utsogoleri, tili ndi anthu amene sakudziwa chomwe akuyenera kuchita, limenero ndi vuto lalikulu. Zosezi ndi kamba koti tikumasankha ndikuyika anthu m’maudindo omwe sakuwayenera ndipo sakudziwa kuti achite chiyani ndi maudindo awowo.

“Vuto lina ndikusagwilitsidwa ntchito bwino kwa ndalama za boma. M’maofesimu mwalembedwa ntchito anthu ambiri omwe samayenera kulembedwa ntchito. Tili ndi ma PS oposa 70, maunduna alipo 18 okha, nde zikutheka bwanji? Ma directors opitilira 400, ku nyumba yachifumu kuli anthu oposa 1000. Talemba anthu ambiri kuyelekeza ndi zomwe tingakwanitse ndi chifukwa chake ndalama yamalipilo ya boma inakwera kwambiri, kuchoka pa K37 biliyoni kufika K110 biliyoni pano,” watelo Kabambe.

Apa Kabambe anapitilira ndikunena kuti ndizovetsa chisoni kuti ndondomeko ya zachuma ya dziko lino imaposa ndalama zomwe dziko lino lingakwanitse kupeza zomwe wati ndizoduka mutu ponena kuti sikoyenera kuti dziko lino nthawi zonse lidzidalira thandizo lochokera mayiko akunja.

Iye watsindika kuti zomwe zikuchitika pano zili ndi kuthekera kowononga dziko lino ponena kuti, “Ana akukanika kupita ku sukulu chosecho akhoza bwinobwino, ku university akusankhidwa ochepa, akasankhidwaso akuyeneraso akadzisakile chakudya komaso pogona. Dziko lino likulephera kusamalira ana ake omwe ndipo tikupanga mavuto adzawoneneni ku m’badwo ukubwerawo chifukwa ambiri mwa anawa akhala osaphunzira bwino.”

Kabambe wadzudzulaso mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ndi nduna zake chifukwa cha ukamwendo njira zomwe wati zikuthandizira kuwononga chuma cha dziko lino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.