Khasala amenyedwa ndi achitetezo a boma ku Nsanje

Advertisement
Nsanje

Achitetezo akunyumba ya boma amenya khansala wachipani cha United Democratic Front (UDF) m’dela la Ruo m’boma la Nsanje, Mariko Mulotali.

Izi zinachitika kum’mawaku pomwe khansalayu anamvedwa akunyoza utsogoleri wachipani cha Malawi Congress (MCP) nthawi yomwe mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera amakhazikitsa ntchito yomanga sukulu zatsopano za Makhanga Primary ndi Makhanga CDSS m’bomalo.

Khansala Mulotali watsimikiza kuti wamenyedwa ndi achitetezowa koma sanafotokoze zambiri zokhudza nkhaniyi.

Poyakhapo pa nkhaniyi, M’neneli wachipani cha MCP, a Jessie Kabwira ati kusamvana komwe kunalipo pakati pambali ziwirizi kunadza kamba koti akhansalawa samazindikiridwa ndi achitetezowa.

Kabwira wati nkhaniyi tsopano yatha ndipo akugwira ntchito limodzi ndi khansalayu pomwe mtsogoleri wadziko lino akuyendera ntchito zachitukuko m’derali.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.