Oimbira mpira wavulazidwa ku Nkhata-Bay

Advertisement
Football

Timu ya Chombe Market Rangers yomwe ikusewera nawo mu mpikisano wa Castel Challenge ili pa chiopsezo choletsedwa kutenga nawo mbali mu mpikisanowu kapena kupatsidwa chindapusa cha ndalama zokwana K500,000 kamba koti osewera a timuyi adamenya komanso kuvulaza oimbira a MacNails Gausi, kutsatira kugonja 2-1 ndi timu ya Chibuku FC masanawa pa bwalo la Maganga. 

Izi zidachitika kutsatira akuluakulu a Chombe Market Rangers atatsutsana ndi kuonjezeredwa kwa mphindi zomwe Gausi adawonjezera pambuyo pa mphindi 90, ponena kuti anzawowo amataya dala nthawi yomwe idakhazikitsidwa.

Malinga ndi Gawo 24 ndime ya 12 ya malamulo oyendetsera mpikisanowu timu yopezeka ndi mlandu womenya oiymbira ikuyenera kulipira chindapusa cha ndalama zokwana K500,000 kapena kuchotsedwa mu mpikisanowu.

Yemwe anali mkulu oyang’anira masewerowa

Salter Mhone, komanso membala wa komiti yoyendetsa masewero a mpira m’boma la NkhataBay ndi omwe adawona izi zikuchitika, Koma wapampando wa komiti ya mpira m’boma la Nkhata Bay, Joseph Mperu, adapempha nthawi kuti aperekepo ndemanga pankhaniyi.

Chombe Market Rangers ikuyembekezeka kusewera ndi Free Movers pofuna kupeza timu imodzi yomwe ipite mu semifinal.

Pakadali pano bungwe loyendetsa masewero ku chigawo chakumpoto ladzuzula mtchitidwewu ndipo lati lidikira ripoti kuti lichite chiganizo chake.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.