Bambo anjatidwa chifukwa chopha munthu

Advertisement
Kasungu

Apolisi m’boma la Kasungu anjata a Yosefe Phiri a zaka 29 ndipo akusaka anzawo ena awiri omwe akuwaganizira kuti anamenya ndi kupha Eleson Phiri ati kamba komuganizra kuti anawatsinkhira nyama ya ku tchire.

Malinga ndi a Miracle Hauli yemwe ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali, a Phiri akuganizilidwa kuti anapha munthuyu ndi anzawo pa 4 mwezi uno m’mudzi mwa Yotamu kwa Nthundwala m’dera la mfumu yaikulu Kawamba.

A Hauli anena kuti woganizilidwayu amagulitsa kachaso ndipo malemuwa anali kasitomala wawo.

Malinga ndi a Hauli, madzulo apa 3 mwezi uno, malemuwa akuti adalowa mchipinda chophikiramo cha woganizilidwayu ndikuba nyama ya ku tchire yomwe imaphikidwa.

“Woganizilidwayu atalowa mchipindachi anazindikira munthu wina wagwira poto yemwe munali nyamayo ndipo anayamba kumenya mothandizana ndi anzake zomwe zinachititsa kuti afe tsiku lotsatira,” tero a Hauli.

Zotsatira za chipatala cha ching’ono cha Mkanda lidaonetsa kuti malemuwa anafa kamba kotaya magazi ochuluka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.