Njala yavuta Ku Machinga, anthu akudya chitedze

Advertisement
Msaka

Phungu wa dera la Machinga Likwenu, a Bright Msaka, wadandaula kuti anthu ena m’boma la Machinga akudya chitedze pomwe njala yafika posauzana m’bomali. 

A Msaka analakhula izi Lolemba Ku Nyumba ya Malamulo.

Malingana ndi a Msaka, anthuwa akumanyika chitedzechi m’madzi kenako n’kuchiswa ndikutenga nthangala zake nkuphika ngati kalongonda.

“Ku Machinga njala yavuta kwambiri ndipo anthu akuvutika, akumagonera chitedze chifukwa chosowa chakudya cholongosoka,” anatero a Msaka.

Iwo anati zomwe zikuchitika ku Machinga chaka chino sizinaonekepo ndi kale lonse.

A Msaka apempha boma kuti lichite changu popeleka thandizo la chakudya kwa anthuwa.

Mfumu ya mdera la Mtumbwinda nayo yatsimikiza za vuto la njala mu dera lake lomwe lafika posautsa.

Mfumuyi yati anthu akukolora chitedze ndicholinga chofuna chakudya pamodzi ndi ana awo.

Malingana ndi Mfumuyi, vuto la njala lavuta Ku Machinga chifukwa choti anthu sanakolore chakudya chokwanira kamba Ka ng’amba yomwe inavuta chaka chino, ndipo anthuwa akudya zakudya zomwe zili zopereka chiopsezo ku miyoyo yawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.