Blue Eagles yathetsa ufumu wa Bullets 

Advertisement
FDH Bank Cup

Timu ya Blue Eagles yakhala akatswiri a chikho cha FDH cha chaka cha 2024 itagonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets 3-2 kudzera m’mapenote pomwe mphindi 90 zinatha opanda mphatso ya chigoli chilichonse.

Masewerawa, omwe anaseweredwa pa bwalo la Bingu, anabweretsa pamodzi likukumwe la ochemelera omwe anasangalara ndi momwe ma team onse awiri anasewelera.

Bullets, yomwe imateteza chikhochi, inayesetsa kuti ipeze chigoli komatu anzawowo nde anachilimika, kutchinjiriza mwa mtima biiii, uku akudzigwetsa kuti masewerowo apite ku mapenote.

 Andrew Juvinala, Ganizani James, komanso Lankeni Mwale adagoletsa ma penote awo, pomwe a Bullets, Gomezgani Chirwa ndi Nickson Nyasulu ndi omwe anagoletsa koma Precious Phiri, Clyde Senaji, ndi Babatunde Adepoju adaphonya zomwe zidapangitsa kuti Blue Eagles ipitilize kusunga mbiri kuti ikakumana ndi Bullets mu ndime yotsiliza ya chikho, simagonja. 

Kupambana kumeneku ndikoyamba kuti timuyi, yomwe ikusewera mu league yaing’ono, ipambane chikho cha dziko lonse la Malawi.

Timuyi kuti ifike mundime yomaliza idatulutsa matimu atatu a Super League, Silver Strikers, Baka City, Karonga United, komanso Santhe Admarc, kuti afike mu ndimeyi. 

Pamene timuyi ikukondwerera kupambana kwawo koyenera, anthu otsatira masewero m’dziko muno akuyembekezera mwachidwi kulandiranso timuyi mu league yaikulu itatuluka mu chaka cha 2023.

ulendo wa ma Eagles kuti mu 2024 ukhale otani.

Timuyi, yomwe eni ake ndi a Polisi, yagonjetsapo Bullets mu mpikisano wa Chibuku, wa Press komanso wa Airtel ndipo lero yamwemwetera mu mpikisano wa FDH.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.