30 million yapelekedwa kwa achinyamata 30 kuti akachitire malonda osiyanasiyana 

Advertisement
Triephornia Mpinganjira

Achinyamata okwana 30 dzulo alandira ndalama zokwana K1 million aliyense kuchokera kwa m’modzi mwa anthu ochita malonda m’dziko muno, Triephornia Thompson Mpinganjira.

Achinyamatawa alandira ndalamayi kuti akayambire malonda osiyana-siyana komanso kupititsa patsogolo malonda awo pansi pa ndondomeko ya ‘Kuthandiza omwe alibe kuthekera kupita patsogolo’.

M’mawu ake, mlendo olemekezeka ku mwambowu a Vera Kamtukule omwe ndi Nduna ya zokopa alendo anayamikira a Mpinganjira pothandiza achinyamatawa ndi Mpamba wa bizinezi. 

Iwo anati ndalama zomwe alandira achinyamata ziwathandiza kusintha miyoyo yawo.

“Zomwe apanga a Mpinganjira ndi zinthu zopambana komanso iwowa awonetsa chikondi pa achinyamata powatukula ndi mpamba omwe awapatsawu. Ndikupempha ena kuti atengerepo phunziro pa zabwino zomwe achita mayiwa,” anetero a Kamtukule.

A Mpinganjira ati ndiokondwa kuti achinyamata ambiri afikilidwa ndi thandizo loti athe kuchita malonda ndi kusintha miyoyo yawo.

A Mpinganjira anatiso iwo apitiliza kuthandiza achinyamata ndi ndalama za bizinezi, chifukwa pafupifupi achinyamata 197, 000 analembera kuti achite nawo mwayi kotero akhale akupitiliza kusankhapo pa achinyamata wo.

M’modzi mwa achinyamata omwe alandira ndalamayi a Hawa Shabir, anathokoza mai Triephornia kamba kopereka mwayi kuti achinyamata akwaniritse masophenya awo. 

Iwo anati ndi okondwa kwambiri kuti wapatsidwa ndalama imeneyi kuti akachitire bizinezi yomwe ndi ya ulimi wa ziweto monga mbuzi.

“Ndine osangalala kwambiri kuti ndili nawo mu m’gulu la achinyamata omwe tapatsidwa ndalama zoti tikapangire ma bizinesi osiyana-siyana. Ine ndalama yomwe ndalandira ipangitsa kuti masomphenya anga atheke omwe ndikukhala mlimi wa ziweto,” anatero a Shabir.

Shabir anapempha achinyamata anzake omwe alandira ndalama yi kuti agwiritse ntchito ndalamayi moyenera. 

Ndondomekoyi yomwe ndi ya ndalama zokwana K34 million ndipo inayamba m’mwezi wa April chaka chino, yakwanitsa kufikira achinyamata 34 a m’madera osiyana-siyana m’dziko muno. 

Achinyamata pafupi-fupi 197,000 ndi omwe analembera mayiwa kuti apeze nawo mwayi wa thandizoli.

A Abbas Nasser, yemwe ndi mkulu wa kampani ya Credible Investment Limited (CIL), yomwe idathandizapo ndi ndalama yokwana K2 million komanso a Thomson Mpinganjira omwe adathandizapo ndi ndalama yokwana K14 million kuti anthu othandizidwa mpamba achuluke, adali nawo pa mwambo opeleka thandizolo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.