Mafuta a galimoto sakuyenera kukwera – Chaponda

Advertisement
Chaponda

Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma mnyumba ya malamulo a George Chaponda wanena kuti kukweza mafuta agalimoto monga momwe lanenera lipoti la komiti yowona za zachilengedwe, ndikuyika miyoyo ya a Malawi pachiswe.

Poyankhura ndi olemba nkhani ku nyumba ya malamulo m’mawawu, Chaponda wati ndizomvetsa chisoni kuti dziko lino likuvutika pa chuma pomwe mtsogoleri wake akuwononga ndalama zambiri kuyenda maiko osiyanasiya.

A Chaponda awuza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti achepetse ma ulendo akunja chifukwa akuwononga ndalama zambiri.

Malinga ndi a Chaponda ndalama za Maulendowa zitha kuthandizira kuletsa chiganizo chokweza mtengo wa mafuta a galimoto m’dziko muno.

“Kukweza mitengo wa mafutawa kutha kukhudza a Malawi ambiri kotero akuyenera kuika njira zopewera kuti Amalawi avutike. Akati akweze mtengowu tidzayamba kuchita zionetsero,” atero a chaponda.

A Chaponda awizanso boma kuti liyambe kugwiritsa ntchito akazembe ake maiko asiyanasiyana kuimila mtsogoleri wa dziko lino kusiyana ndikuyenda komwe kukuwononga ndalama za nkhaninkhani.

Polakhulapo a Sameer Suleman anenetsa kuti iwo achita ziwonetsero ngati Boma likweza Mafuta.

A Suleman akuti sangalole kuti a Malawi omwe akuvutika kale pano apitilize kuvutika chifukwa cha kukwezedwa Kwa mafuta.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.