Zakunyumba ya malamulo: amphungu a DPP ayatsa makandulo pokumbukira Chilima

Advertisement
Parliament

Pomwe nkhani yokhudza lipoti la ngozi ya ndege yatenga malo, a phungu a chipani cha Democratic Progressive lero anayatsa makandulo mnyumba ya malamulo pofuna kukumbukira yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima yemwe anafa pangoziyi pamodzi ndi ena asanu ndi atatu.

Izi zinachitika pomwe aphunguwa amapita kupumulira pomwe anamaliza zokambirana za muchigawo chakumawa. Makandulo ali m’manja, aphunguwa amayimba nyimbo zoyamikira malemu Chilima.

Izi zikuchitika pomwe kum’mawa lero mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma a George Chaponda anapempha boma kuti libweletse poyera lipoti la kafukufuku wa chomwe chidagwetsa ndege yomwe malemu Chilima ndi ena 8 adakwera popita ku maliro a Ralph Kasambara.

PaKadali pano, boma kudzera kwa nduna ya zofalitsa nkhani Moses kunkuyu atsutsa mphekesera zomwe zikuveka kuti kampani yomwe idapanga kafukufuku wa ngozi ya ndegeyi BFU, idatulutsa zotsatira za kafukufuku wake.

Kunkuyu wati ili ndibodza lankunkhuniza ndipo wati kampani ya BFU ukuchitabe kafukufuku wake ndipo wati boma lidzabweretsa poyera lipotili likadzatulutsidwa. 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.