Mzibambo obaya mayi ake oyembekezera akaseweza jere

Advertisement
Malawi24

Mzibambo wa zaka 21 zakubadwa, wagamulidwa kukagwira ukaidi kwa zaka zisanu kamba kobaya mayi wake woyembekezera ndikupha mwana yemwe amayemnekezeredwayo. 

Malingana ndi woyimilira boma pa mulanduwu a Mussa Samuteni, mzibambo wopanda chisoniyu yemwe wazindikilidwa kuti ndi Happy Banda, wamangidwa posachedwapa atabaya mayi wake woyembekezerawa ndi mpeni pamimba.

Izi zapangitsa kuti bwalo la milandu la Nkhunga ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota-li limugamule kukakhala ku ndende zaka zisanu pamlandu wovulaza munthu.

Malingana ndi a Samuteni, mwana yemwe mayiyu amayembekezera wamwaliranso, pamene mayi wovulazidwayu akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Kamuzu Central munzinda wa Lilongwe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.