Dzizimba! Bambo wamangidwa atanyamula bokosi lamaliro usiku

Advertisement
Neno

Bambo wina m’boma la Neno wamangidwa pomwe mzake wathawa kamba kopezeka atasenza mabokosi a maliro usiku omwe akuti sing’anga wina anawauza kuti asandutsidwa magalimoto.

Malingana ndi lipoti la polisi lomwe tawona, womangidwayu ndi Christopher Manyika, wazaka 42 yemwe anamangidwa Lolemba sabata ino cha m’ma 11 koloko usiku pomwe wothawayo wazindikilidwa ngati Henry Kapakasa.

Lipotili likusonyeza kuti m’modzi mwa apolisi m’bomalo, Blessings Chikwatu, anatsinidwa khutu kuti oganiziridwa awiriwa adanyamula mabokosi a maliro kuchokera kunyumba kwawo kupita nawo pa bwalo la masewero la Chifenthe pakati pausiku.

Potsatira kutsinidwa khutuku, a Chikwatu pamodzi ndi apolisi ena anathamangira ku bwalo la masewero la Chifenthe komwe adapeza awiriwa aliyese ataseza bokosi lamaliro, ndipo akuti amafuna achite za matsenga.

Awiriwa atazindikira kuti pamalopo pafika apolisi, adapomya mabokosiwa pansi ndikuliutsa liwiri la mtondo wadooka, koma Manyika adagwidwa ndi kumangidwa pomwe Kapakasa adakwanitsa kuthawa.

Atamufunsa zomwe zimachitika, Manyika adaulula kuti sing’anga wina ndi yemwe adawalamula kuti achite mwikhowu ponena kuti mabokosi amalirowo omwe munalibe kanthu asandutsidwa magalimoto omwe akhale awo.

Malingana ndi lipotili, apolisi pakadali pano akhazikitsa ntchito yosaka woganizilidwa othawayo komaso sing’anga yemwe adawalamura kuchita zonsezi. 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.