Nyumba ya Malamulo isintha nsalu ya mipando

Advertisement
Malawi Parliament

Mipando ya kunyumba ya malamulo ayiveka nsalu yatsopano. Poyamba nyumbayi idali ndi mipando ya blue ndipo pano aikutira nsalu ina yomwe ndi mbendera ya dziko lino.

Mipando mnyumbayi, ndiyomwe ija yakale koma yangokutilidwa nsalu ina ndipo mbali ina ya mpandowo ikuonekabe blue.

Pa 17 November 2023 Ishmael Onani, phungu wa dera la ku m’mwera m’boma la Dedza anapempha nyumba ya malamulo, kuti isinthe makaka a mipando ya mu nyumba ya malamulo.

Onani, anati makaka a mipando a nyumbayi omwe ndi a blue , akuyenela kusinthidwa ndikukhala ndi makaka a mbendela ya dziko lino.

Mipando ina yokhala alendo, yomwe ili mmwamba, siidakutilidwe nsalu yatsopanoyo.

Mu nyumbayi ayikamoso  ti makanema tomwe tili m’mipando ya phungu aliyense.

Lero a phungu ayamba zokambirana Mnyumbayi zomwe zikuyembekeza kuzatha pa 20 September 2024.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.